Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 23

Kodi Mabuku Athu Amalembedwa ndi Kumasulidwa Bwanji?

Kodi Mabuku Athu Amalembedwa ndi Kumasulidwa Bwanji?

Dipatimenti Yolemba Mabuku, ku U.S.A.

Ku South Korea

Ku Armenia

Ku Burundi

Ku Sri Lanka

Kuti nchito yathu yolalikila “uthenga wabwino . . . kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu ulionse” icitike bwino, timafalitsa mabuku m’zinenelo zopitilila 750. (Chivumbulutso 14:6) Kodi timakwanitsa bwanji kucita nchito yaikulu imeneyi? Timakwanitsa cifukwa ca thandizo la olemba amene ali m’maiko osiyana-siyana ndi omasulila odzipeleka. Onse amenewa ni Mboni za Yehova.

Pokonza nkhani, amalemba m’Cizungu. Bungwe Lolamulila limayang’anila Dipatimenti Yolemba Mabuku kumalikulu athu. Dipatimenti imeneyi imayang’anila nchito ya olemba amene ali kumalikulu ndi m’maofesi a nthambi zina. Kukhala ndi olemba osiyana-siyana kumatithandiza kulemba nkhani za anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana. Cifukwa ca zimenezi, mabuku athu amafika pamtima anthu a m’maiko osiyana-siyana.

Nkhani zikalembedwa, amazitumiza kwa otembenuza. Pambuyo pakuti nkhani yolembedwa aiŵelenga ndi kuivomeleza, amaitumiza pakompyuta kwa otembenuza padziko lonse, kuti akaitembenuze ndi kuona ngati zimene atembenuza zili bwino, ndi kuiŵelenganso. Iwo amayesetsa kusankha “mau olondola a coonadi” amene m’cinenelo cao, adzapeleka tanthauzo lonse la Cizungu.—Mlaliki 12:10.

Nchito imafulumila ndi makompyuta. Kompyuta singalembe nkhani ndi kutembenuza yokha. Komabe, mwa kugwilitsila nchito makompyuta, nchito ya olemba ndi otembenuza imafulumila. Mboni za Yehova zinapanga pulogalamu ya pakompyuta yochedwa Multilanguage Electronic Publishing System (MEPS). Imeneyi imawalola kulemba mau m’zinenelo zosiyana-siyana, kuikamo zithunzi-thunzi, ndi kukonza nkhanizo kuti akazisindikize.

Kodi n’cifukwa ciani timacita khama conco, kutembenuza ngakhale zinenelo zing’ono-zing’ono? Cifukwa n’cifunilo ca Yehova kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.”—1 Timoteyo 2:3, 4.

  • Kodi nchito yolemba mabuku athu imacitika bwanji?

  • N’cifukwa ciani timatembenuza mabuku athu m’zinenelo zambili?