KUCEZA NA | ANTONIO DELLA GATTA
N’cifukwa Ciani Wansembe Anasiya Cipembedzo Cake?
ANTONIO DELLA GATTA anacita maphunzilo aunsembe ku Rome kwa zaka 9. Kenako mu 1969 anaikidwa kukhala wansembe. Patapita nthawi anakhala mkulu pasukulu ina ya ansembe yomwe ili pafupi na mzinda wa Naples ku Italy. Ali kumeneko, anacita kafukufuku pa zomwe cipembedzo ca Katolika cimaphunzitsa ndipo anaona kuti si zocokela m’Baibo. Mtolankhani wa Galamuka! anaceza naye kuti adziwe zambili za moyo wake.
Kodi munabadwila kuti?
N’nabadwila ku Italy m’caka ca 1943. M’banja mwathu tinalimo ana 7 ndipo tinali a Katolika. Tinali kukhala m’mudzi winawake waung’ono. Bambo anga anali mlimi komanso kalipentala.
N’ciani cinakupangitsani kukhala wansembe?
Nili mnyamata, n’nali kumamvetsela ansembe akulalikila, zinali kunisangalatsa kwambili. N’nali kucita cidwi na mmene mawu awo anali kumvekela komanso miyambo yomwe anali kucita. Zimenezi zinapangitsa kuti niyambe kuganiza zodzakhala wansembe. Nili na zaka 13, mayi anga ananipititsa kusukulu yogonela komweko yomwe inali kuphunzitsa anyamata kuti adzakhale ansembe.
Kodi kusukuluko munali kuphunzilanso Baibo?
Osati kwenikweni. Nili na zaka 15, aphunzitsi anga ena ananipatsa Kabaibo kokhala na Mauthenga Abwino okha basi ndipo n’nali kuŵelenga kangapo. N’tafika zaka 18, n’napita ku Rome kukaphunzila pa yunivesite inayake yomwe imayang’anilidwa na papa. N’nali kuphunzila Cilatini, Cigiriki, mbili yakale, filosofe, komanso maphunzilo a zacipembedzo. Tinali kunena mavesi a m’Baibo omwe tinaloweza komanso tinali kumvetsela Baibo ikuŵelengedwa pa maulaliki a pa Sondo. Komabe sininganene kuti tinali kuphunzila Baibo.
Ndiyeno mutakhala wansembe munali kuphunzitsanso anthu?
Nthawi zina n’nali kuphunzitsa zomwe nauzidwa na akulu-akulu a ku Vatican. Koma nthawi zambili n’nali kugwila nchito ya mu ofesi.
N’cifukwa ciani munayamba kukayikila zomwe cipembedzo ca Katolika cimaphunzitsa?
Pali zinthu zitatu zimene zinali kunikayikitsa. Coyamba, chalichici cimalowelela ndale. Caciŵili, cimalekelela akulu-akulu ake akamacita makhalidwe oipa. Ndipo cacitatu, zinthu zina zimene chalichici cimaphunzitsa, sizicokela m’Baibo. Mwacitsanzo, zingatheke bwanji kuti Mulungu, yemwe ni wacikondi azilanga anthu powawocha m’moto kwamuyaya? Komanso kodi n’zoona kuti Mulungu amafuna kuti tizingobweleza pemphelo lomwelomwelo kambili-mbili pogwilitsa nchito korona?
Ndiye munatani?
N’napemphela kwa Yehova kuti anithandize, misozi ili mbwe-mbwe-mbwe. N’nagulanso Baibo inayake yacikatolika yomwe inali itangosindikizidwa kumene m’Citaliyana ndipo ninayamba kuiŵelenga. Kenako Sondo lina m’mawa titamaliza mwambo wa Misa, a Mboni aŵili anafika kumene n’nali kukhala. Tinaceza kwanthawi ndithu ndipo tinakambilana zokhudza Baibo komanso zimene imaphunzitsa pa nkhani ya cipembedzo coona.
N’ciani cinakucititsani cidwi na Mbonizo?
N’nacita cidwi na mmene anali kulankhulila akamafotokoza mavesi a m’Baibo yanga ija. Anali kuoneka kuti amakhulupilila na mtima wonse zomwe Baibo imanena ndipo anali kufotokoza mosatekeseka. Kenako n’nayamba kuphunzila Baibo na wa Mboni wina, dzina lake Mario. Iye anali woleza mtima ndipo anali kubwela Loweluka lililonse ca m’ma 9 koloko m’maŵa, zivute zitani.
Kodi ansembe ena anatani ataona kuti mukuphunzila ni a Mboni?
Analibe nazo cidwi kwenikweni. N’napempha ena kuti tiziphunzilila limodzi, koma palibe amene anapitiliza. Koma ineyo n’nali kusangalala kwambili na zimene n’nali kuphunzila. N’napeza yankho la funso lomwe linali kunizunguza mutu kwa nthawi yaitali. Funso lake linali loti, ‘N’cifukwa ciani Mulungu amalola kuti anthufe tizivutika komanso kuti zoipa zizicitika padzikoli?’
Kodi akulu-akulu a cipembedzo canu sanakuletseni kuphunzila Baibo?
Mu 1975, n’napita kangapo konse ku Rome kukawafotokozela maganizo anga. Akulu-akuluwa anayesetsa kuniuza kuti nisinthe maganizo, koma palibe anagwilitsa nchito Baibo. Kenako pa 9 January 1976, n’nalemba kalata yowauza kuti si inenso Mkatolika. Patatha masiku aŵili n’nacoka kumene n’nali kukhala kuja n’kukwela sitima kupita kukasonkhana na a Mboni za Yehova. Poyamba sin’nali kudziŵa kuti msonkhanowo ni waukulu, womwe pamakhala mipingo ya Mboni za Yehova yambili. Zimene n’naona pamsonkhanowo zinali zosiyana kwambili na zomwe zinali kucitika kuchalichi kwathu. Pafupifupi onse anali na Baibo ndipo wokamba nkhani akachula vesi, aliyense anali kutsegula Baibo yake n’kumatsatila akamaŵelenga.
Kodi acibale anu anatani atamva zimenezi?
Ambili sanasangalale nazo ndipo anali kunitsutsa koopsa. Koma kenako n’namva kuti mng’ono wanga wina anali kuphunzilanso na a Mboni m’cigawo ca Lombardy. N’napita kukamuona ndipo a Mboni a kumeneko ananithandiza kupeza nchito komanso malo okhala. Kumapeto kwa caka comweco n’nabatizika n’kukhala wa Mboni za Yehova.
Nikuona kuti nili pa ubwenzi wabwino na Mulungu
Kodi mumanong’oneza bondo na zomwe munacitazi?
Ayi ndithu. N’kuona kuti nili pa ubwenzi wabwino na Mulungu cifukwa n’kumudziŵa bwino kucokela pa zomwe ndaphunzila m’Baibo, osati pongotengela nzelu za anthu kapena miyambo yacipembedzo. Panopa nikamaphunzitsa anthu nimasangalala cifukwa nimadziŵa kuti zomwe n’kuwaphunzitsazo n’zoona.