Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GALAMUKA! Na. 1 2021 | Nzelu Zokuthandizani Kukhala na Umoyo Wacimwemwe

Tonsefe timafuna kukhala na umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa. N’zotheka kupeza nzelu zokuthandizani kukhala na umoyo waconco. Ŵelengani kuti muone mmene mungapezele nzelu zimenezo.

 

Nzelu Zokuthandizani Kukhala na Umoyo Wacimwemwe

Mulungu wamphamvuzonse amapeleka malangizo anzelu otithandiza kukhala na umoyo wacimwemwe palipano, komanso kutsogolo.

Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe

Kodi amuna, akazi, makolo, na ana angacite ciani kuti m’banja mwawo mukhale cimwemwe?

Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendele na Anthu Ena

Ni makhalidwe ati amene angatithandize kukhalabe mwamtendele na anthu ena?

Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila

N’ciani cimathandiza kuti munthu akhale na umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa?

N’cifukwa Ciani Timavutika, Kukalamba, na Kufa?

Onani zinthu zinayi zikulu-zikulu zimene zimapangitsa kuti tizivutika, kukalamba, na kufa.

Ziphunzitso Zimene Zimatipatsa Ciyembekezo

Malonjezo a Mulungu amatipatsa ciyembekezo ca kutsogolo. Onankoni mmene zinthu zidzakhalila malonjezowo akadzakwanilitsidwa.

Cidziŵitso Cimene Cimatithandiza Kukhala Mabwenzi a Mulungu

Kodi Baibo imatiuza ciani za Mulungu, zimene zingakusonkhezeleni kufuna kum’dziŵa na kukhala naye paubwenzi?

N’zotheka Kupeza Nzelu

N’zotheka imwe kupeza nzelu zocokela kwa Mulungu, ndipo iye akukupemphani kuti mupindule na nzeluzo. Kodi mudzatelo?

Kodi Mungakonde Kudziŵa Zambili?

Ngati n’conco, pali mavidiyo, mavidiyo a tukadoli, mbali za kufunsa mafunso, na nkhani zimene zingakuthandizeni kupanga zisankho zabwino komanso kukhala na banja lacimwemwe.