Nzelu Zokuthandizani Kukhala na Umoyo Wacimwemwe
“Nimamva cisoni nikaona zoipa zimene zimacitika padzikoli, monga nkhondo, umphawi, matenda, na kuzunzidwa kwa ana. Ngakhale n’conco, nili na ciyembekezo.”—RANI. *
Rani anapeza cimwemwe ceniceni ataphunzila za Mlengi wathu, Mulungu wamphamvuzonse, amene ni Gwelo la nzelu zenizeni. Pamene muŵelenga nkhani zotsatilazi, onani mmene ziphunzitso zake zingakuthandizileni . . .
kukhala na banja lacimwemwe
kukhala mwamtendele na anthu ena
kukhala wokhutila
kudziŵa cifukwa cake timavutika komanso kufa
kukhala na ciyembekezo codalilika ca tsogolo labwino
kum’dziŵa bwino Mlengi wathu na kukhala naye paubwenzi
Mudzaonanso kuti Mlengi wathu amapeleka nzelu kwa aliyense amene amazifuna-funa, osati kwa anthu oŵelengeka cabe.
^ ndime 2 Maina m’magazini ino asinthidwa.