KWA MAKOLO
8: Citsanzo
ZIMENE CIMATANTHAUZA
Makolo amene amapeleka citsanzo cabwino, amacita zimene amaphunzitsa. Mwacitsanzo, simungayembekezele mwana wanu kuti azikamba zoona ngati amakumvelani mukamba kuti, “Auze kuti nacokapo,” pamene simufuna kukamba na munthu wina amene wabwela pakhomo panu.
“Anthu ambili amakonda kukamba kuti, ‘Uzicita zimene nimakamba, osati zimene nimacita.’ Koma zimenezi sizikhala zothandiza kwa ana. Ana ali monga thonje. Thonje limayamwa zilizonse zamadzi zimene mwaliikamo. Nawonso ana amatengela zilizonse zimene timakamba na kucita, ndipo akaona kuti zimene timacita sizigwilizana ndi zimene timawaphunzitsa, iwo amatiuza.”—David.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Iwe amene umalalikila kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?”—Aroma 2:21.
CIFUKWA CAKE N’COFUNIKA
Ana ang’ono-ang’ono, kuphatikizapo azaka pakati pa 13 ndi 19, amatengela kwambili makolo awo kuposa wina aliyense, ngakhale anzawo. Izi zitanthauza kuti makolo muli pa malo abwino kwambili otsogolela ana anu m’njila yoyenela malinga ngati mucita zimene mumawaphunzitsa.
“Tikhoza kupeleka malangizo kwa mwana mobweleza-bweleza n’kuyamba kukaikila ngati iye amasungadi zimene timamuuza. Koma tsiku limene tidzalephela kucita zimene timakamba, iye adzatiuza kuti sitinacite zimene timamuuza. Ana amaona zilizonse zimene timacita, olo pamene ise tiona monga kuti sanaone.”—Nicole.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Nzelu yocokela kumwamba [ndi] . . . “yopanda cinyengo.”—Yakobo 3:17.
ZIMENE MUNGACITE
Dzifufuzeni kuti muone mfundo zimene m’mayendela. Kodi imwe mumakonda kutamba zosangalatsa zabwanji? Kodi mumacita naye bwanji zinthu mnzanu wa m’cikwati komanso ana anu? Kodi muli na anzanu a makhalidwe otani? Kodi mumaganizila ena? Mwacidule, kodi mungakonde ana anu kutengela citsanzo canu?
“Ine na amuna anga sitimakakamiza ana athu kucita zinthu zimene ise sitimacita.”—Christine.
Muzipepesa mukalakwitsa. Ana anu amadziŵa kuti ndimwe opanda ungwilo. Conco, pamene mukamba kuti “pepani” kwa mnzanu wa m’cikwati komanso kwa ana anu ngati mwalakwitsa, ndiye kuti mupeleka citsanzo cabwino cokhala oona mtima ndi odzicepetsa.
“Ana athu amafunika kuona kuti timavomeleza tikalakwitsa komanso timapepesa. Ngati siticita zimenezi, iwo adzaphunzila kubisa zolakwa zawo.”—Robin.
“Monga makolo tili pa malo abwino kwambili othandiza ana athu. Ndipo citsanzo cathu cabwino ndiye cida camphamvu kwambili cimene tili naco, cifukwa nthawi zonse amaona mmene timacitila zinthu. Pamene aona zimene ise makolo timacita mu umoyo, zimakhala monga kuti nthawi zonse akuphunzitsidwa.”—Wendell.