GALAMUKA! Na. 2 2020 | Mafunso 5 Pankhani ya Mavuto Ayankhidwa.
Aliyense wa ife amakhudzidwa na mavuto aakulu monga matenda, ngozi, matsoka a zacilengedwe, kapena zaciwawa.
Anthu amafuna kudziŵa cifukwa cake timavutika.
Ena amakamba kuti mavuto amabwela cifukwa zinalembedwelatu, conco amaona kuti palibe kweni-kweni zimene tingacite kuti tiwapewe.
Enanso amakamba kuti timavutika cifukwa ca zina zimene tinacita kumbuyoku mu umoyo uno, kapena mu umoyo wina tisanamwalile na kubadwanso.
Tsoka likacitika, anthu amakhala na mafunso ambili.
Zimene Ena Amakhulupilila
Onani zifukwa zosiyana-siyana zimene zipembedzo zimapeleka ponena za cifukwa cake timavutika.
1 Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?
Anthu amasoceletsedwa na ziphunzitso zabodza ponena za Mulungu. Kodi zoona ni ziti?
2 Kodi Ife Eni Ndiye Timapangitsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?
Ngati yankho ni inde, ndiye kuti ungakhale udindo wathu kucepetsako mavuto.
3 N’cifukwa Ciani Anthu Abwino Nawonso Amavutika?
Baibo itithandiza kupeza yankho.
4 Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?
Kodi Mulungu amene analenga zinthu zokongola angalole kuti anthufe tizivutika? Ngati yankho ni iyai, kodi cinalakwika n’ciani?
5 Kodi Mavuto Adzatha?
Baibo imatiuza bwino-bwino mmene Mulungu adzacotselapo mavuto.
Thandizo Ilipo
Ngakhale kuti mavuto athu aoneke monga sadzatha, pali citsogozo codalilika cimene cingatithandize.