Muzilemekeza Amene Afunika Kulandila Ulemu
“Iye wokhala pampando wacifumu, ndi Mwanawankhosa, atamandidwe ndiponso alandile ulemu, ulemelelo, ndi mphamvu, kwamuyaya.”—CHIV. 5:13.
1. N’cifukwa ciani ena amafunika kupatsidwa ulemu? Nanga m’nkhani ino tidzaphunzila ciani?
KULEMEKEZA munthu kumatanthauza kumuona kukhala wofunika ndi kum’patsa ulemu. Munthu amapatsidwa ulemu cifukwa ca zimene wacita kapena cifukwa cakuti ali ndi udindo wina-wake wapadela. Conco, tingafunse kuti, N’ndani amene tiyenela kulemekeza? Ndipo n’cifukwa ciani afunika kulemekezedwa?
2, 3. (a) N’cifukwa ciani Yehova ndiye woyenela kulemekezedwa koposa? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Kodi Mwanawankhosa wochulidwa pa Chivumbulutso 5:13 n’ndani? Ndipo n’cifukwa ciani ni woyenela kulandila ulemu?
2 Malinga n’zimene lemba la Chivumbulutso 5:13 limakamba, “wokhala pampando wacifumu, ndi Mwanawankhosa” afunikadi kulemekezedwa. Caputa 4 ca buku limeneli la m’Baibo cimafotokoza cifukwa cimodzi cimene cipangitsa Yehova kukhala woyenela kulandila ulemu. Cimakamba za zolengedwa zauzimu za kumwamba zimene zimafuula potamanda Yehova, “amene adzakhalabe ndi moyo kwamuyaya.” Zolengedwazo zimafuula kuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”—Chiv. 4:9-11.
Yoh. 1:29) Baibo imakamba kuti Yesu ni wapamwamba kwambili kuposa mafumu onse kapena anthu onse amene anakhalapo mafumu. Imafotokoza kuti: “Iye amene ali Mfumu ya olamulila monga mafumu ndi Mbuye wa olamulila monga ambuye, . . . Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, amene amakhala m’kuwala kosafikilika. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.” (1 Tim. 6:14-16) Kunena zoona, palibe mfumu ina iliyonse imene inadzipeleka kutifela monga dipo la macimo athu. Zimenezi ziyenela kutilimbikitsa kulemekeza Mwanawankhosa mogwilizana ndi zolengedwa zoculuka zakumwamba zimene zimafuula kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa ndiye woyenela kulandila mphamvu, cuma, nzelu, nyonga, ulemu, ulemelelo, ndi madalitso.”—Chiv. 5:12.
3 Mwanawankhosayo ni Yesu Khristu. Iye ndiye “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akucotsa ucimo wa dziko.” (4. N’cifukwa ciani kulemekeza Yehova na Khristu n’kofunika kwambili?
4 Kulemekeza Yehova ndi Khristu n’kofunika kwambili. Kuti tidzakhale na moyo wosatha tifunika kucita zimenezi. Mau a Yesu a pa Yohane 5:22, 23 amamveketsa bwino mfundo imeneyi. Iye anati: “Atate saweluza munthu aliyense, koma wapeleka udindo wonse woweluza kwa Mwana, kuti onse alemekeze Mwana monga mmene amalemekezela Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamutuma.”—Ŵelengani Salimo 2:11, 12.
5. N’cifukwa ciani munthu aliyense afunika kupatsidwa ulemu?
5 Anthu analengedwa “m’cifanizilo ca Mulungu.” (Gen. 1:27) Conco, munthu aliyense, pamlingo winawake amaonetsa makhalidwe a Mulungu. Mwacitsanzo, anthu amatha kukondana, kucitilana cifundo, ndi kukomelana mtima. Cinanso n’cakuti anthufe tinalengedwa na cikumbumtima. Cikumbumtima cimeneci, ngakhale kuti nthawi zina cimakhala copotoka, cimatithandiza kudziŵa cabwino ndi coipa, kapena colungama ndi cosalungama. (Aroma 2:14, 15) Anthu ambili amakonda zinthu zaukhondo ndi zokongola. Komanso amafuna kukhala mwamtendele ndi ena. Modziŵa kapena mosadziŵa, iwo amaonetsako mbali ya ulemelelo wa Yehova. Pa cifukwa cimeneci, munthu aliyense afunika kupatsidwa ulemu.—Sal. 8:5.
KUPELEKA ULEMU WOYENELELA KWA ENA
6, 7. Pankhani yolemekeza ena, kodi Mboni za Yehova zimasiyana bwanji na anthu ena?
6 Tifunika kukhala osamala kuti tipewe kulemekeza anthu ena mopambanitsa. Anthu ambili amasonkhezeledwa ndi mzimu wa dziko la Satana pankhani imeneyi. N’cifukwa cake amakonda kutamanda anthu ena mopambanitsa m’malo mowapatsa ulemu woyenelela. Iwo amatamanda kwambili atsogoleli acipembedzo, andale, akatswili a zamaseŵela, ndi ena, ndipo amafika powaona monga ni milungu. Zotulukapo zake n’zakuti acicepele ndi acikulile omwe amayamba kutengela kavalidwe kawo, kakambidwe kawo, kapena zocita zawo.
7 Akhristu oona amapewa kupeleka ulemu waconco kwa anthu ena. Pa anthu onse amene anakhalako padziko lapansi, Khristu yekha ndiye anapeleka citsanzo cangwilo cimene tiyenela kutengela. (1 Pet. 2:21) Mulungu sangasangalale ngati ife tipeleka ulemu wopambanitsa kwa anthu. Tifunika kukumbukila kuti: “Onse ndi ocimwa ndipo ndi opelewela pa ulemelelo wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Conco, sitiyenela kupatsa munthu wina aliyense ulemu wopambanitsa ngati kuti tikumulambila.
8, 9. (a) Kodi Mboni za Yehova zimawaona bwanji olamulila a boma? (b) Pankhani yomvela olamulila, kodi malile athu ni ati?
8 M’dzikoli, anthu ena ali na udindo Aroma 13:1, 7.
wolamulila. Akulu-akulu a boma ali na udindo wolimbikitsa anthu kutsatila malamulo ndi kukhala mwamtendele, ndiponso kusamalila nzika za dziko lawo. Zimene amacita zimapindulitsa aliyense. N’cifukwa cake mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti ayenela kugonjela atsogoleli a boma monga “olamulila akuluakulu.” Iye anawalangiza kuti: “Pelekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho . . . Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.”—9 M’pake kuti Mboni za Yehova zimapeleka ulemu woyenelela kwa olamulila a boma mogwilizana ndi cikhalidwe ca kumaloko. Timalabadila akatipatsa malamulo kapena malangizo enaake. Koma timawalemekeza ndi kuwamvela mogwilizana ndi mfundo za m’Malemba. Sitiwamvela mpaka kufika pophwanya malamulo a Mulungu kapena kutengako mbali pa nkhani za ndale.—Ŵelengani 1 Petulo. 2:13-17.
10. Kodi atumiki akale a Yehova anapeleka citsanzo cotani pankhani yomvela ndi kulemekeza boma ndi olamulila?
10 Atumiki a Yehova akale anapeleka citsanzo cabwino pankhani yolemekeza ndi kumvela olamulila. Pamene Ufumu wa Roma unapeleka lamulo lakuti anthu akalembetse m’kaundula, Yosefe ndi Mariya analabadila. Iwo anapita ku Betelehemu ngakhale kuti panthawiyo Mariya anali pafupi kubeleka mwana wake woyamba. (Luka 2:1-5) Nthawi ina, pamene Paulo anaimbidwa mlandu, anadzichinjiliza mwaulemu ndi kupeleka ulemu woyenelela kwa Mfumu Herode Agiripa ndi Fesito, bwanamkubwa waciroma woyang’anila cigawo ca Yudeya.—Mac. 25:1-12; 26:1-3.
11, 12. (a) Pankhani yopeleka ulemu, n’cifukwa ciani timafunika kusiyanitsa pakati pa olamulila a boma ndi atsogoleli acipembedzo? (b) Kodi panakhala zotulukapo zanji pamene Mboni ina ya ku Austria inaonetsa ulemu kwa mtsogoleli wina wandale?
11 Komabe, ife Mboni za Yehova timapewa kupeleka ulemu wapadela kwa atsogoleli acipembedzo, ngakhale kuti iwo angafune kuti ticite zimenezo. Cipembedzo conama cimaipitsa dzina la Mulungu ndi kupotoza zimene Mau ake amakamba. Conco, atsogoleli acipembedzo sitiwapatsa ulemu wapadela, koma timawaona monga anthu ena onse. Kumbukilani kuti Yesu anadzudzula atsogoleli acipembedzo a m’nthawi yake ndi kuwauza kuti ndi atsogoleli akhungu ndi acinyengo. (Mat. 23:23, 24) Koma ngati tipeleka ulemu woyenelela kwa olamulila a boma, pangakhale zotulukapo zabwino, mwinanso zimene sitinali kuyembekezela.
12 Mwacitsanzo, Leopold Engleitner anali Mboni ya Yehova yacangu ya ku Austria. Iye anamangidwa ndi asilikali a Nazi, ndipo anamutenga m’sitima kupita naye ku ndende yochedwa Buchenwald. M’sitimayo munalinso Dr. Heinrich Gleissner, amene anali mmodzi wa akaidi. Asanamangidwe, Dr. Gleissner anali mmodzi wa atsogoleli andale ku Austria. Koma boma la Nazi linali kudana naye. Pa ulendowo, M’bale Engleitner anafotokoza cikhulupililo cake mwaulemu kwa Gleissner, ndipo iye anamvetsela mwacidwi. Pambuyo pa nkhondo yaciŵili ya pa dziko lonse, Gleissner mobweleza-bweleza anagwilitsila nchito udindo wake kuthandiza Mboni za ku Austria. Mwina mukumbukila zitsanzo zina zoonetsa mapindu amene amabwela ngati Mboni za Yehova zipeleka ulemu woyenelela kwa olamulila a boma, mogwilizana ndi zimene Baibo imakamba.
ANTHU ENA OFUNIKA KUWAPATSA ULEMU
13. N’ndani maka-maka woyenela kupatsidwa ulemu? Ndipo n’cifukwa ciani?
13 Abale ndi alongo athu auzimu tiyenela kuwalemekeza, maka-maka akulu amene amatsogolela mumpingo. (Ŵelengani 1 Timoteyo 517) Abale amenewa timawalemekeza Aef. 4:8) Ganizilani za akulu mumpingo, oyang’anila madela, a m’Komiti ya Nthambi, ndi a m’Bungwe Lolamulila. Abale na alongo a m’zaka 100 zoyambilila anali kulemekeza kwambili amuna osankhidwa amene anali kuwatsogolela, ndipo nafenso timacita cimodzi-modzi. Komabe sititamanda mopambanitsa abale odziŵika kwambili amene amatsogolela mumpingo wacikhristu. Komanso tikawaona, siticita zinthu monga kuti taona mngelo. Ngakhale n’conco, timawalemekeza abale amenewa cifukwa cakuti amatumikila mwakhama ndipo ni odzicepetsa.—Ŵelengani 2 Akorinto 1:24; Chivumbulutso 19:10.
mosasamala kanthu kuti ndi olemela kapena osauka, ophunzila kapena osaphunzila, kapena kuti acokela ku dziko liti. Baibo imakamba kuti abale amenewa ni “mphatso za amuna.” Amuna amenewa amacita mbali yofunika kwambili pa nchito yosamalila anthu a Mulungu. (14, 15. Fotokozani kusiyana pakati pa abusa oona acikhristu ndi anthu amene amadzicha kuti ndi abusa.
14 Akulu amenewa ndi abusa auzimu odzicepetsa. Popeza ni odzicepetsa, amakana kulemekezedwa mopambanitsa monga anthu ochuka a m’dzikoli. Mwanjila imeneyi, iwo amasiyana ndi atsogoleli ambili azipembedzo amakono ndi a m’zaka 100 zoyambilila. Ponena za atsogoleli acipembedzo a m’zaka 100 zoyambilila, Yesu anati: “Amakonda malo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso kupatsidwa moni m’misika.”—Mat. 23:6, 7.
15 Abusa oona acikhristu amalabadila modzicepetsa mau a Yesu akuti: “Koma inu musamachulidwe kuti Rabi, cifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. Komanso musamachule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi, wakumwamba Yekhayo. Musamachedwe ‘atsogoleli,’ pakuti Mtsogoleli wanu ndi mmodzi, Khristu. Koma wamkulu kwambili pakati panu akhale mtumiki wanu. Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.” (Mat. 23:8-12) Conco, n’zosadabwitsa kuti Mboni za Yehova m’mipingo yosiyana-siyana padziko lonse, zimalemekeza akulu ndi kuwakonda.
16. N’cifukwa ciani tifunika kucita khama kuti timvetsetse na kutsatila mfundo za m’Baibo pankhani yolemekeza ena?
16 Pangatenge nthawi kuti tidziŵe ulemu woyenelela umene tiyenela kupeleka kwa ena ndi mmene tingaupelekele. Ni mmenenso zinalili kwa Akhristu oyambilila. (Mac. 10:22-26; 3 Yoh. 9, 10) Koma tifunika kuyesetsa kutsatila mfundo za m’Baibo pa nkhani ya kulemekeza ena. Kucita zimenezi kumabweletsa mapindu ambili.
MAPINDU AMENE TIMAPEZA NGATI TIPELEKA ULEMU WOYENELELA KWA ENA
17. Kodi pamakhala mapindu anji ngati tilemekeza anthu amene ali pa udindo?
17 Ngati tilemekeza olamulila aboma, iwo angatilole kupitiliza kugwila nchito yolalikila mwaufulu. Nthawi zambili, zotulukapo zake zimakhala zakuti anthu amaona kuti zimene timacita n’zabwino. Zaka zingapo zapitazo, mpainiya wina wa ku Germany, dzina lake Birgit, anapita kukapezeka pa mwambo wa otsiliza maphunzilo pamene mwana wake wamkazi anatsiliza maphunzilo. Matica anauza Birgit kuti cinali cokondweletsa ndi conyaditsa kuphunzitsa ana a Mboni pa sukuluyo. Iwo anakambanso kuti cikanakhala cocititsa manyazi pasukuluyo pakanakhala popanda ana a Mboni. Ndiyeno Birgit anawafotokozela kuti: “Timaphunzitsa ana athu kutsatila mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino, ndipo kucita zimenezi kumaphatikizapo kulemekeza atica.” Tica wina anati: “Ana onse akanakhala ngati anu, sembe nchito yophunzitsa siivuta.” Patapita mawiki angapo, mmodzi wa maticawo anapezeka pa msonkhano wacigawo ku Leipzig.
18, 19. N’cifukwa ciani kupeleka ulemu woyenelela kwa akulu n’kofunika?
18 Pamene tilemekeza akulu mumpingo, tifunika kutsatila mfundo za cilungamo ndi zothandiza zopezeka m’Mau a Mulungu. (Ŵelengani Aheberi 13:7, 17.) Tifunika kuwayamikila pa nchito yaikulu imene amacita ndi kuyesetsa kumvela malangizo amene amatipatsa. Kucita zimenezi kungawathandiza kupitiliza kucita utumiki wawo mokondwela. Koma izi sizitanthauza kuti tifunika kutengela ndendende ciliconse cimene mkulu winawake amacita, monga kakambidwe kake ka nkhani, kavalidwe kake, mmene amadzikonzela, kapena mmene amakambila ndi anthu. Kucita zimenezi kungapeleke cithunzi colakwika. Tiyenela kukumbukila kuti nayenso ni munthu wopanda ungwilo. Munthu amene tifunika kutengela monga citsanzo cathu ni Khristu.
19 Ngati tipeleka ulemu woyenelela kwa akulu, m’malo mowatamanda monga anthu ochuka a m’dzikoli, ndiye kuti tikuwathandiza. Cimakhala cosavuta kwa iwo kupewa mzimu wonyada, wodziona monga ofunika kwambili kapena olungama ngako.
20. Kodi kupeleka ulemu woyenelela kwa ena kumatithandiza bwanji?
20 Kulemekeza anthu amene afunika kupatsidwa ulemu, kumatithandiza kuti tisakhale odzikonda. Kumatithandizanso kupewa kudzikweza ngati anthu ena atilemekeza. Cinanso, kulemekeza ena moyenelela kumatithandiza kuti tiziyendela pamodzi ndi gulu la Yehova, limene limapewa kutamanda anthu mopambanitsa, kaya ni Mboni kapena ayi. Komanso kumatithandiza kuti tisakhumudwe ngati munthu wina amene tinali kum’lemekeza wacita cinacake colakwika.
21. Ndi phindu lalikulu liti limene limakhalapo ngati tipeleka ulemu woyenelela kwa amene afunikila ulemu?
21 Phindu lalikulu kwambili limene timapeza ngati tipeleka ulemu woyenelela kwa ena n’lakuti timakondweletsa mtima wa Mulungu. Timaonetsa kuti ndife omvela ndiponso okhulupilika kwa iye, ndipo kucita zimenezi kumathandiza kuti Mulungu ayankhe amene amamutonza. (Miy. 27:11) Anthu ambili m’dzikoli ali na maganizo olakwika pankhani yolemekeza ena. Koma ife tili na mwayi ngako cifukwa tadziŵa mmene tingalemekezela ena mogwilizana ndi malangizo a Yehova.