Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8

Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Athu?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Athu?

Kodi nthawi zina mumakayikila zakuti Mulungu amamva mapemphelo anu? Ngati n’conco, si imwe mwekha. Anthu ambili apemphelapo kwa Mulungu kuti awathandize pa vuto linalake, koma silinathe. Kodi zimenezi zionetsa kuti Mulungu samvetsela mapemphelo athu? Iyai! Baibo imatitsimikizila kuti Mulungu amamvetsela mapemphelo athu ngati timupempha m’njila yoyenela. Tiyeni tione zimene Baibo imakamba.

MULUNGU AMAMVETSELA.

“Inu Wakumva pemphelo, anthu a mitundu yonse adzabwela kwa inu.”—Salimo 65:2.

Anthu ena amakamba kuti amapemphela cifukwa amaona kuti pemphelo limawathandiza kumvelako bwino, olo kuti sakhulupilila zakuti pali winawake amene amawamvetsela. Koma sikuti pemphelo ni njila cabe yotithandiza kuti timveleko bwino ndiponso kuti tikwanitse kupilila mavuto ayi. Baibo imatitsimikizila kuti “Yehova * ali pafupi ndi onse oitanila pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’coonadi. . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Salimo 145:18, 19.

Conco, tisakayikile kuti Yehova Mulungu amamva mapemphelo ya anthu amene amamulambila. Mwacikondi, iye anati: “Mudzaitanila pa ine komanso mudzabwela ndi kupemphela kwa ine ndipo ine ndizakumvetselani.”—Yeremiya 29:12.

MULUNGU AMAFUNA KUTI MUZIPEMPHELA KWA IYE.

“Limbikilani kupemphela.”—Aroma 12:12.

Baibo imatilimbikitsa kuti ‘tizipemphela mosalekeza.’ Imatinso ‘tizipemphela pa cocitika ciliconse.’ Telo n’zoonekelatu kuti Yehova Mulungu amafuna kuti tizipemphela kwa iye.—Mateyu 26:41; Aefeso 6:18.

N’cifukwa ciani Mulungu amafuna kuti tizipemphela kwa iye? Ganizilani izi: Kodi tate samakondwela ngati mwana wake wamng’ono wam’pempha thandizo? Amakondwela. N’zoona kuti tateyo angakhale kuti akudziŵa kale zimene mwanayo akufunikila kapenanso mmene amvelela. Koma akamvela mwana akupempha thandizo, amaona kuti mwanayo amam’dalila ndiponso amam’konda. N’cimodzi-modzi na ife. Tikapemphela kwa Yehova Mulungu, iye amaona kuti timamudalila na kum’konda.—Miyambo 15:8; Yakobo 4:8.

MULUNGU AMASAMALA KWAMBILI ZA IMWE.

‘Mutulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

Mulungu amafuna kuti tizipemphela kwa iye cifukwa amatikonda ndiponso amatidela nkhawa. Iye amadziŵa bwino mavuto athu na nkhawa zathu, ndipo amafuna kutithandiza.

Pa umoyo wake wonse, Mfumu Davide anali kupempha thandizo kwa Yehova Mulungu. Analinso kumuuza maganizo ake na mmene anali kumvelela. (Salimo 23:1-6) Kodi Mulungu anamuona bwanji Davide? Anamukonda ndipo anamvetsela mapemphelo ake ambiliwo. (Machitidwe 13:22) Mofananamo, Mulungu amamvetsela mapemphelo athu cifukwa amatikonda.

“YEHOVA AMAMVA MAWU ANGA”

Awa ni mawu a mmodzi wa olemba buku la m’Baibo la Masalimo. Iye anali kukhulupilila kuti Mulungu anali kumva mapemphelo ake, ndipo kudziŵa zimenezi kunamuthandiza kwambili. Anaona kuti ali pafupi na Mulungu, komanso anapeza mphamvu zomuthandiza kupilila zinthu zosautsa komanso zomvetsa cisoni.—Salimo 116:1-9.

Ngati timakhulupilila kuti Mulungu amamva mapemphelo athu, sitidzaleka kupemphela kwa iye. Ganizilani citsanzo ca Pedro, amene amakhala kumpoto kwa dziko la Spain. Mwana wake wamwamuna wa zaka 19 anamwalila pa ngozi yapamsewu. Polila, Pedro anakhuthulila Mulungu za mumtima mwake. Anamupempha mobweleza-bweleza kuti amutonthoze na kumuthandiza. Kodi n’ciani cinacitika? Iye anati: “Yehova anayakha mapemphelo anga kupitila mwa Akhristu anzanga. Iwo ananitonthoza na kunithandiza pamodzi na mkazi wanga.

Nthawi zambili Mulungu amayankha mapemphelo athu kupitila mwa mabwenzi acikondi. Iwo amatitonthoza na kutithandiza

Olo kuti mapemphelo ake sanapangitse kuti mwanayo auke, anamuthandiza kwambili Pedro na banja lake. Mkazi wake, María Carmen, anati: “Kupemphela kunanithandiza kupilila imfa ya mwana wanga. N’nadziŵa kuti Yehova Mulungu anali kumvetsela cifukwa nikapemphela kwa iye, mtima unali kukhala m’malo ndiponso n’nali kukhala na mtendele wa mumtima.”

Zimene Baibo imakamba komanso zimene anthu ambili aona pa umoyo wawo, zimaonetselatu kuti zoona Mulungu amamva mapemphelo. Komabe, n’zoonekelatu kuti Mulungu sayankha mapemphelo onse. N’cifukwa ciani amayankha mapemphelo ena koma ena ayi?

^ ndime 5 Yehova ni dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.