Kodi Mudziŵa?
N’cinthu cacilendo citi cimene Yesu anacitila anthu akhate?
Ayuda akale anali kuopa khate limene linali lofala m’nthawi imeneyo. Nthenda yoopsa imeneyi inali kuwononga minyewa ya munthu wodwalayo n’kumupundula. Kunalibe mankhwala ocilitsa khate pa nthawiyo. M’malomwake, amene anali kudwala matendawa, anali ndi udindo wodziŵitsa ena kuti ali na khate.—Levitiko 13:45, 46.
Atsogoleli acipembedzo Aciyuda anapanga malamulo awo okamba za mocitila ndi akhate, amene m’Malemba mulibe. Malamulo amenewa anapangitsa kuti anthu odwala khate azivutika kwambili. Mwacitsanzo, malamulo a Arabi anali kunena kuti anthu sayenela kuyandikila munthu wodwala khate mpaka kufika pa mtunda wa mamita aŵili. Ndipo ngati mphepo ikukuntha, anthu anafunika kukhala pa mtunda osacepela mamita 45 kucokela pamene pali munthu wakhate. Malemba amakamba kuti odwala khate afunika kukhala “kunja kwa msasa”. Koma olemba Talmud ena anamasulila mawu amenewa kuti odwala khate afunika kukhala kunja kwa mzinda. Conco, m’Rabi wina wake akaona munthu wakhate mumzinda, anali kumuponya miyala ndi kumuuza kuti: “Pita ku malo ako, usadetse anthu kuno.”
Koma Yesu sanacite zimenezo. M’malo mowapitikitsa anthu odwala khate, nthawi zina anali kuwagwila ngakhale kuwacilitsa kumene.—Mateyu 8:3.
Ni mfundo ziti zimene atsogoleli acipembedzo Aciyuda anali kutsatila pofuna kuthetsa cikwati?
M’zaka 100 zoyambilila, atsogoleli azipembedzo anali kutsutsana pa nkhani yothetsa cikwati. Conco panthawi ina, Afarisi ena anafunsa Yesu funso ili: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa cifukwa ciliconse?”—Mateyu 19:3.
Cilamulo ca Mose cinali kuvomeleza mwamuna kuleka mkazi wake ngati “wam’peza ndi vuto linalake.” (Deuteronomy 24:1) M’nthawi ya Yesu, panali masukulu aŵili a Arabi amene anali kuphunzitsa zinthu zosiyana ndi lamulo limeneli. Sukulu yapamwamba ya Shammai inamasulila lemba limeneli kuti cifukwa cimodzi cokha cothetsela cikwati ndi kucita “codetsa,” kutanthauza cigololo. Koma, Sukulu ya Hillel inakamba kuti mwamuna angathetse cikwati cake mwalamulo ngati ayambana na mkazi wake, ngakhale pa nkhani zing’ono-zing’ono. Sukulu imeneyi inakambanso kuti, mwamuna angathetse cikwati ngati mkazi wanyetsa ndiyo kapena nsima kapena akaona mkazi wina wokongola kwambili.
Nanga Yesu anayankha bwanji funso limene Afarisi anamufunsa? Iye anayankha mosapita mbali kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatila wina wacita cigololo, kupatulapo ngati wamusiya cifukwa ca dama.”—Mateyu 19:6, 9.