Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Kodi Mulungu amayankha mapemphelo onse?
KODI MUNGAKAMBE KUTI AMAYANKHA MAPEMPHELO . . .
A munthu aliyense
A anthu ena
Sayankha
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
“Yehova ali pafupi ndi onse . . . amene amamuitana m’coonadi.”—Salimo 145:18.
MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
Mulungu sayankha mapemphelo a anthu amene samumvela. (Yesaya 1:15) Koma anthu a conco ‘angakhalenso pa ubwenzi wabwino’ na Mulungu ngati asintha makhalidwe awo.—Yesaya 1:18.
Kuti Mulungu ayankhe pemphelo, lifunika kukhala logwilizana na zimene iye amafuna, ndipo zimene amafunazo zipezeka m’Baibo.—1 Yohane 5:14.
Kodi tifunika kukhala bwanji popemphela?
ANTHU ENA AMAKHULUPILILA kuti nthawi zonse tifunika kugwada, kuŵelama, kapena kuika manja pamodzi popemphela. Inu muganiza bwanji?
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
Mulungu anayankha mapemphelo a anthu amene anapemphela ali ‘cokhala pansi,’ ‘coimilila,’ ‘cogona’ kapena ‘cogwada.’ (1 Mbiri 17:16; 2 Mbiri 30:27; Ezara 10:1; Machitidwe 9:40) Iye safuna kuti tikhale mwanjila inayake yapadela popemphela.
MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
Mulungu amamvela mapemphelo a anthu odzicepetsa.—Salimo 138:6.
Mungapemphele ca mumtima ndiponso m’cinenelo ciliconse.—2 Mbiri 6:32, 33; Nehemiya 2:1-6.