Kodi Mudziŵa?
Kodi anthu ochulidwa m’Baibo anali kudziŵa bwanji poyambila caka kapena mwezi?
KWA Ayuda okhala M’dziko Lolonjezedwa, caka cinali kuyamba na nyengo yolima komanso yobyala, imene masiku ano ni September kapena October.
Anthu anali kuŵelengetsela utali wa mwezi malinga na kuculuka kwa masiku amene mwezi ukuonekela kumwamba, pafupi-fupi masiku 29 kapena 30. Koma poŵelengetsela caka, anali kugwilitsa nchito kayendedwe ka dzuŵa. Komabe, akaŵelengetsela caka pogwilitsa nchito mwezi, cakaco cinali kukhala cofupikilapo. Zikatelo, anali kufunika kupeza njila yoŵelengetsela nthawi kuti pasakhale kusiyana. Njila yake inali kuwonjezela masiku kapena mwezi wina apa na apo, mwina caka cotsatila cisanayambe. Izi zinali kuthandiza kuti kalenda igwilizane na nyengo yobyala komanso yokolola.
Koma m’nthawi ya Mose, Mulungu anauza anthu ake kuti caka copatulika ciziyamba na mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, masiku ano ndiwo March kapena April. (Eks. 12:2; 13:4) M’mwezi umenewu anali kucita cikondwelelo ca kukolola balele.—Eks. 23:15, 16.
Katswili wina wa Baibo, Emil Schürer, anati: “Sicinali covuta anthu kudziŵa nthawi yowonjezela mwezi wina pa kalenda. Cikondwelelo ca Pasika, cimene ciyenela kucitika mwezi ukakhala wathunthu, m’mwezi wa Nisani (pa Nisani 14), ciyenela kucitika pamene utali wa usana na usiku zalingana . . . Komabe, ngati cakumapeto kwa caka zadziŵika kuti Pasika idzafika tsiku lake lisanakwane, Ayuda anali kuwonjezela mwezi wina [wa nambala 13], mwezi wa Nisani usanafike.”
Mboni za Yehova zimayendela njila imeneyi pofuna kudziŵa tsiku locita Mgonelo wa Ambuye, pa Nisani 14, poyendela kalenda ya Ciheberi. Mipingo padziko lonse lapansi imauzidwa za tsiku limeneli pasadakhale. *
Kodi Aheberi anali kudziŵa bwanji kuti mwezi watha, watsopano wayamba? Masiku ano, zimenezi n’zosavuta kudziŵa cifukwa umangoyang’ana pa kalenda. Koma kwa anthu ochulidwa m’Baibo sizinali zopepuka.
Pa nthawi ya Cigumula, miyezi inali kukhala na masiku 30. (Gen. 7:11, 24; 8:3, 4) M’kupita kwa nthawi, pa kalenda ya Ciheberi mwezi sunali kungokhala wa masiku 30. Mwacitsanzo, mwezi watsopano unali kuyamba akangoona kuti mwezi wakhala, pambuyo pa masiku 29 kapena 30 a mwezi wapita.
Pa nthawi ina, ponena za kuyamba kwa mwezi watsopano, Davide na Yonatani anati: “Mawa ndi tsiku lokhala mwezi.” (1 Sam. 20:5, 18) Conco, zioneka kuti podzafika m’ma 1000 B.C.E., miyezi anali kuiŵelengetsela pasadakhale. Koma kodi Aisiraeli anali kudziŵa bwanji kuti mwezi watsopano wayamba? Zolemba zina zaciyuda zokhudza malamulo na miyambo zimatithandiza kupeza yankho. Zimaonetsa kuti Ayuda atacoka mu ukapolo ku Babulo, Sanihedirini (Khoti Yapamwamba ya Ayuda) ndiyo inali kuŵelengetsela nthawi. M’mwezi wa 7 uliwonse wocita zikondwelelo, a khoti imeneyi anali kukumana pa tsiku la 30 la mweziwo. A khotiwo ndiwo anali kunena pamene mwezi wotsatila udzayamba. Kodi iwo anali kudziŵa bwanji zimenezi?
Alonda amene anali kukhala pamwamba pa mpanda wozungulila Yerusalemu, anali kuyang’ana kumwamba usiku kuti aone ngati mwezi wakhala. Mwezi ukangokhala, anali kudziŵitsa a khoti amenewo. Ndipo a khotiwo akakhutila na malipoti amene apelekedwa akuti mwezi waonekela, anali kulengeza kuti mwezi watsopano wayamba. Koma bwanji ngati mitambo kapena nkhungu yachinga alondawo moti sanathe kuona bwino-bwino kuti mwezi wakhala? Zikakhala conco, mwezi wosathawo unali kukhala wa masiku 30, ndiyeno mwezi watsopano unali kuyamba.
Zolemba za Ayudazo zinafotokoza kuti pofuna kupeleka cilengezo cakuti mwezi watsopano wayamba, anali kuyatsa moto pamwamba pa phili la Maolivi, pafupi na Yerusalemu. Ndiyeno pa malo enanso okwela kuzungulila Isiraeli, moto unali kuyatsidwa monga cilengezo kwa anthu onse. Pakapita nthawi, amithenga anali kutumidwa kuti akalengeze zimenezo. Conco, Ayuda ku Yerusalemu komanso a kumadela ena, anali kudziŵitsidwa kuti mwezi watsopano wayamba. Izi zinali kuwathandiza kuti acite zikondwelelo panthawi imodzi.
Mungaone chati yotsatilayi kuti ikuthandizeni kudziŵa miyezi, zikondwelelo, komanso nyengo m’nthawi ya Aisiraeli.
^ Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1990, tsa. 15, komanso nkhani yakuti, “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga,” mu Nsanja ya Mlonda yacizungu ya June 15, 1977.