Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 43

Mulungu ‘Adzakupatsani Mphamvu’​—Motani?

Mulungu ‘Adzakupatsani Mphamvu’​—Motani?

“[Yehova] adzakulimbitsani, ndi kukupatsani mphamvu.”—1 PET. 5:10.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi Mulungu anali kuwalimbikitsa bwanji atumiki ake akale?

 NTHAWI zambili mawu a Mulungu amachula anthu okhulupilika kuti ni amphamvu. Koma ngakhale aja amene anali amphamvu kwambili si nthawi zonse pamene anali kudzimva telo. Nthawi zina Mfumu Davide anali kudzimva “wamphamvu ngati phili,” koma nthawi zina anali kudzimva wofooka ndipo anali “kucita mantha.” (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali na mphamvu zapadela pamene mzimu wa Mulungu unali kugwila nchito pa iye, iye anazindikila kuti popanda mphamvu zocokela kwa Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:​5, 6; 16:17) Amuna okhulupilika amenewa anali olimba cifukwa Yehova ndiye anawapatsa mphamvu.

2. N’cifukwa ciyani mtumwi Paulo ananena kuti anali wofooka komanso wamphamvu? (2 Akorinto 12:​9, 10)

2 Mtumwi Paulo anadziŵa kuti nayenso anafunikila mphamvu zocokela kwa Yohova. (Ŵelengani 2 Akorinto 12:​9, 10.) Monga ambili a ife, mtumwi Paulo nayenso anali kulimbana na mavuto a thanzi. (Gal. 4:​13, 14) Nthawi zina, zinalinso zovuta kuti acite coyenela. (Aroma 7:​18, 19) Analinso kukhala na nkhawa pa zimene zidzamucitikila. (2 Akor. 1:​8, 9) Komabe, pamene anali wofooka, m’pamene anali kukhala wamphamvu. Motani? Cifukwa Yehova anam’patsa mphamvu zimene anali kufunikila kuti apilile mavuto ake.

3. Kodi nkhani ino iyankha mafunso ati?

3 Nafenso Yehova amatilonjeza kuti adzatipatsa mphamvu. (1 Pet. 5:10) Koma sitingalandile mphamvuzo ngati siticitapo kanthu. Tifanizile motele, injini imapangitsa kuti galimoto iziyenda. Koma kuti galimoto iyende, dalaiva ayenela kuponda giya. Mofananamo, Yehova ni wokonzeka kutipatsa mphamvu zimene tifunikila. Koma kuti tilandile mphamvuzo, tiyenela kucitapo kanthu. Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti zimene zingatithandize kukhala amphamvu? Nanga tiyenela kucita ciyani kuti tilandile mphamvuzo? Tidzapeza mayankho a mafunso amenewa pamene tikambilana mmene Yehova analimbikitsila anthu atatu ochulidwa m’Baibo—mneneli Yona, Mariya amayi ake a Yesu, komanso mtumwi Paulo. Tionenso mmene Yehova wapitilizila kulimbitsa atumiki ake masiku ano m’njila yofananayo.

MUNGAPEZE MPHAMVU MWA KUPEMPHELA NA KUŴELENGA

4. Tingacite ciyani kuti tilandile mphamvu kucokela kwa Yehova?

4 Njila imodzi imene tingapezele mphamvu zocokela kwa Yehova ni mwa kupemphela kwa iye. Yehova angayankhe mapemphelo athu mwa kutipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7) Cina, tingalimbikitsidwe mwa kuŵelenga mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. (Sal. 86:11) Uthenga wa Yehova kwa ife umatipatsa ‘mphamvu.’ (Aheb. 4:12) Mukapemphela kwa Yehova na kuŵelenga mawu ake, mudzapeza mphamvu zimene mufunikila kuti mupilile, mukhalebe acimwemwe, kapena kukwanilitsa utumiki wovuta. Tiyeni tikambilane mmene Yehova analimbikitsila mneneli Yona.

5. N’cifukwa ciyani Yona anafunikila mphamvu?

5 Mneneli Yona anafunika kulimba mtima. Iye anathaŵa utumiki wovuta umene Yehova anam’patsa. Zotsatila zake n’zakuti anaika moyo wake pa ciopsezo, komanso wa anthu amene anali nawo m’boti pamene cimphepo cinawomba pa nyanja. Oyendetsa boti atam’ponya m’nyanja, cinsomba cacikulu cinam’meza. Iye anadzipeza m’mimba mwa cinsomba, malo oopsa kwambili. Kodi muganiza Yona anamva bwanji? Kodi anaganiza kuti adzafela mmenemo? Kapena anaona kuti Yehova amukana? Yona ayenela kuti anacita mantha kwambili.

Potengela citsanzo ca mneneli Yona, tingapeze bwanji mphamvu pamene tilimbana na mavuto? (Onani ndime 6-9)

6. Malinga na Yona 2:​1, 2, 7, n’ciyani cinalimbikitsa Yona ali m’mimba mwa cinsomba?

6 Kodi Yona anatani kuti apeze mphamvu pamene anali yekha-yekha m’mimba mwa cinsomba? Anapemphela kwa Yehova. (Ŵelengani Yona 2:​1, 2, 7.) Ngakhale kuti Yona sanamvele Yehova, iye analapa ndipo anali wotsimikiza kuti Yehova adzamvela pemphelo lake. Cina, anasinkhasinkha Malemba amene anaŵelenga. N’cifukwa ciyani tikutelo? Pemphelo yake imene ili pa Yona caputala 2, ili na mawu ambili ofanana na amene ali m’buku la Salimo. (Mwacitsanzo, yelekezelani Yona 2:​2, 5 na Salimo 69:1; 86:7.) N’zoonelatu kuti Yona anali kuwadziŵa bwino Malemba amenewa. Ndipo mwa kuwasinkhasinkha anakhala wotsimikiza kuti Yehova adzam’thandiza. Pambuyo pake, Yehova anamupulumutsa m’mimba mwa cisomba, ndipo anali wokonzeka kukwanilitsa utumiki umene anapatsidwa.—Yona 2:10–3:4.

7-8. Kodi m’bale wina wa ku Taiwan anapeza bwanji mphamvu panthawi ya mavuto?

7 Citsanzo ca Yona cingatithandize pamene tikulimbana na mavuto osiyana-siyana. Mwacitsanzo, m’bale Zhiming b wa ku Taiwani, ali na matenda aakulu. Kuwonjezela pamenepo, a m’banja lake amam’citila nkhanza cifukwa ca cikhulupililo cake mwa Yehova. Amapeza mphamvu zocokela kwa Yehova mwa kupemphela na kuŵelenga. Iye anati “Nthawi zambili nikakumana na mavuto, nimakhala na nkhawa moti zimanivuta kucita phunzilo la ine mwini.” Koma samalefuka. Iye anawonjezela kuti “Coyamba, nimapemphela kwa Yehova. Ndiyeno, nimaika mahedifoni na kuyamba kumvetsela nyimbo za Ufumu. Nthawi zina nimaimba nyimbozo cam’munsi-munsi mpaka mtima utakhala m’malo, kenako nimayamba kuŵelenga.”

8 Kucita phunzilo la munthu mwini, kwalimbitsa m’bale Zhiming m’njila imene sanayembekezele. Mwacitsanzo, atacitidwa opaleshoni yaikulu, manesi anamuuza kuti, cifukwa cakucepekela kwa maselo ofiila a m’magazi, angafunike kuikidwa magazi. Usiku wakuti maŵa acitidwa opaleshoni, m’bale Zhiming anaŵelenga za mlongo wina amene anacitidwa opaleshoni yofanana na yake. Maselo ofiila a m’magazi a mlongoyo anali ocepa kwambili poyelekezela na a m’bale Zhiming, komabe anakana kuikidwa magazi, ndipo anacila. Cocitikaco, cinalimbikitsa m’bale Zhiming kukhalabe wokhulupilika.

9. Mungacite ciyani ngati mayeso akufooketsani? (Onaninso cithunzi.)

9 Kodi mumacita mantha kufotokozela Yehova m’pemphelo mmene mukumvela mukamakumana na mavuto? Kapena kodi mumalefuka n’kulephela kuŵelenga? Kumbukilani kuti Yehova amamvetsa mmene mukumvela. Conco, ngakhale mutapeleka pemphelo lacidule, mungakhale otsimikiza kuti iye adzakupatsani zonse zimene mufunikila. (Aef. 3:20) Ngati n’zovuta kwa inu kuŵelenga cifukwa ca kudwala, kutopa, kapena nkhawa, bwanji osangotsatila kuŵelengedwa kwa Baibo kongomvetsela kapena cofalitsa cina? Mungapindulenso na kumvetsela imodzi mwa nyimbo zathu kapena kuonelela vidiyo pa jw.org. Mukamapemphela kwa Yehova na kufuna-funa mayankho a mapemphelo anu m’zinthu zauzimu zimene iye watipatsa, adzakupatsani mphamvu.

PEZANI MPHAMVU KUCOKELA KWA ALAMBILI ANZANU

10. Kodi abale na alongo athu amatilimbikitsa bwanji?

10 Yehova angaseŵenzetse abale na alongo athu kuti atilimbitse. Iwo ‘angatithandize na kutilimbikitsa’ tikakumana na mavuto, kapena pamene tikuyesetsa kucita utumiki wovuta. (Akol. 4:​10, 11) Timafunikila mabwenzi maka-maka “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Tikalefulidwa, alambili anzathu angatithandize mwa kutipatsa ulangizi na kutilimbikitsa kuti tipitilzebe kutumikila Yehova. Tiyeni tione mmene Mariya a mayi ake a Yesu anapezela mphamvu kucokela kwa ena.

11. N’cifukwa ciyani Mariya anafunikila mphamvu?

11 Mariya anafunikila mphamvu. Tangoganizilani nkhawa yaikulu imene anakhala nayo pamene analandila udindo waukulu kucokela kwa mngelo Gabirieli. Iye anali wosakwatiwa, koma anali kudzakhala na mimba. Cina, anali asanalelepo mwana, koma anali kudzalela mwana amene anali kudzakhala Mesiya. Ndipo popeza anali namwali, kodi akanafotokoza bwanji nkhaniyi kwa Yosefe amene anali kufuna kum’kwatila?—Luka 1:​26-33.

12. Malinga na Luka 1:​39-45, kodi Mariya analandila bwanji mphamvu zimene anali kufunikila?

12 Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu zoti akwanilitse utumiki wapadela komanso wovuta umenewo? Anapempha thandizo kwa ena. Mwacitsanzo, iye anapempha mngelo Gabirieli kuti amuuze zowonjezeleka zokudza utumiki umenewo. (Luka 1:34) Posakhalitsa, Mariya anayenda ulendo wautali n’kupita “kudela lamapili” kudziko la Yuda kuti akaone wacibale wake Elizabeti. Ulendo umenewu unam’pindulila ngako. Elizabeti anayamikila Mariya, ndipo mouzilidwa na Yehova anakamba ulosi wolimbikitsa ponena za mwana amene anali kudzabadwayo. (Ŵelengani Luka 1:​39-45.) Mariya anakamba kuti Yehova “wacita zamphamvu ndi dzanja lake.” (Luka 1:​46-51) Yehova analimbikitsa Mariya kupitila mwa mngelo Gabirieli, komanso Elizabeti.

13. Kodi mlongo wa ku Bolivia anapidula bwanji atapempha thandizo kwa alambili anzake?

13 Mofanana na Mariya, inunso mungapeze mphamvu kucokela kwa alambili anzanu. Mlongo wina wa ku Bolivia dzina lake Dasuri anafunikila mphamvu. Atate ake atawapeza na matenda osacilitsika, iye anadzipeleka kuti aziwasamalila kucipatala. (1 Tim. 5:4) Koma kucita zimenezi sikunali kopepuka. Iye anavomeleza kuti, “Nthawi zambili n’nali kuona kuti sindingakwanitse kupitiliza.” Poyamba sanaganize zopempha thandizo kwa ena. Iye anafotokoza kuti, “Sin’nafune kuvutitsa abale na alongo, koma n’naganiza kuti, ‘Yehova adzanipatsa thandizo limene likufunikila.’ Koma pambuyo pake, n’nazindikila kuti posapempha thandizo n’nali kuyesa kulimbana na mavutuwo panekha.” (Miy. 18:1) Dasuri anaganiza zolembeleko mabwenzi ake ena uthenga, na kuwafotokozela mmene zinthu zinali. Ndiyeno iye anati, “sindingathe kufotokoza cilimbikitso cimene n’nalandila kucokela kwa alambili anzanga. Iwo anali kutibweletsela cakudya kucipatala, ndipo anali kuniŵelengela Malemba olimbikitsa. N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti sitili tokha. Tili m’banja lalikulu la Yehova limene ni lokonzeka kutithandiza, kulila nafe, komanso kutilimbikitsa kuti titumikilebe Yehova.”

14. N’cifukwa ciyani tiyenela kulandila thandizo locokela kwa akulu?

14 Njila imodzi imene Yehova amatipatsila mphamvu ni kupitila mwa akulu. Iwo ni mphatso zimene Yehova amagwilitsa nchito potilimbikitsa na kutitsitsimula. (Yes. 32:​1, 2) Conco, mukakhala na nkhawa afotokozeleni akulu. Muzilandila thandizo lawo moyamikila. Yehova angakulimbikitseni kupitila mwa iwo.

CIYEMBEKEZO CANU CA MTSOGOLO CINGAKULIMBIKITSENI

15. Kodi Akhristu onse ali na ciyembekezo canji camtengo wapatali?

15 Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cingatipatse mphamvu. (Aroma 4:​3, 18-20) Pokhala Akhristu, tili na ciyembekezo ca mtengo wapatali codzakhala m’paradiso pano pa dziko lapansi, kapena cokakhala kumwamba. Ciyembekezo cathu cimeneci cimatilimbikitsa kupilila mavuto, kulalikila uthenga wabwino, komanso kucita mautumiki osiyani-siyani mu mpingo. (1 Ates. 1:3) Ciyembekezo cimeneci n’cimene cinalimbikitsa mtumwi Paulo.

16. N’cifukwa ciyani mtumwi Paulo anafunikila mphamvu?

16 Paulo anafunikila mphamvu. M’kalata yake kwa Akorinto, iye anadziyelekezela na ciwiya cosalimba coumbidwa na doti. Iye ‘anapanikizidwa,’ ‘kuthedwa nzelu,’ ‘kuzunzidwa,’ komanso ‘kugwetsedwa pansi.’ Ndipo moyo wake weniweniwo unali pacipsezo. (2 Akor. 4:​8-10) Paulo analemba mawuwa paulendo wake wacitatu waumishonale. Mwina sanali kudziŵa kuti anali kudzakumananso na mavuto ena. Anali kudzacitilidwa ciwawa, kumangidwa na kuikidwa m’ndende, komanso ngalawa kumuswekela pa nyanja.

17. Malinga na 2 Akorinto 4:​16-18, n’ciyani cinalimbikitsa mtumwi Paulo kupilila mayeso?

17 Paulo anapeza mphamvu zopilila mwakuika maganizo pa ciyembekezo cake. (Ŵelengani 2 Akorinto 4:​16-18.) Iye anauza Akorinto kuti, ngakhale kuti thupi lake linali ‘kutha,’ sadzalola zimenezo kumufooketsa. Iye anaika maganizo ake pa zamtsogolo. Ciyembekezo ca Paulo cokakhala na moyo wamuyaya kumwamba, ‘cinali kukulila-kulila,’ moti anali wokozeka kupilila mavuto ali onse omwe akanakumana nawo. Paulo anali kusinkhasinkha za ciyembekezo cimeneco. Conco anayamba kudziona kuti “akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku.”

18. Kodi ciyembekezo ca zamtsogolo calimbikitsa bwanji Tihomir na banja lake?

18 Tihomir, m’bale wa ku Bulgaria, amapeza mphamvu mwa kuganizila za ciyembekezo cake. Zaka zingapo m’mbuyomo, mng’ono wake Zdravko anamwalila pa ngozi ya pamsewu. Kwanthawi yaitali, m’bale Tihomir anavutika na cisoni cacikulu. Kuti apilile, iye na banja lake amayelekeza mmene ciukitso cidzakhalile. Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zina timakambilana kumene tidzakumana naye, zakudya zimene tikam’pikila, amene tidzakaitana kumaceza athu oyamba akadzaukitsidwa, komanso zimene tidzamuuza zokhudza masiku otsiliza.” Tihomir anafotokoza kuti, kuika maganizo pa ciyembekezo kumalimbikitsa banja lake kupitilizabe kupilila, na kuyembekeza nthawi pamene Yehova adzaukitsa m’bale wake.

Kodi mumaona kuti umoyo wanu udzakhala bwanji m’dziko latsopano? (Onani ndime 19) c

19. Mungacite ciyani kuti mulimbikitse ciyembekezo canu? (Onaninso cithunzi.)

19 Kodi mungalimbikitse bwanji ciyembekezo canu? Mwacitsanzo, ngati muli na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi, muziŵelenga Malemba amene amafotokoza mmene Paradaiso adzakhalile na kuwasinkhasinkha. (Yes. 25:8; 32:​16-18) Muziganizila mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano. Yelekezelani kuti muli m’dzikolo. Kodi mukuona ndani? Mukumva ciyani? Nanga mumvela bwanji? Kuti kuyelekezaku kukhale kwaphindu, muziona mapikica a Paradaiso m’zofalitsa zathu, kapena mungaonelele mavidiyo a nyimbo zakuti, Dziko Latsopano Likubwelalo, Dziko Latsopano ili Pafupi Kwambili, kapena Ganizila Moyo Wam’tsogolo. Tikamaganizila kwambili za ciyembekezo cathu ca dziko latsopano tidzaona mavuto athu kuti ni “akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Yehova adzakupatsani mphamvu kupitila mu ciyembekezo cimene wakupatsani.

20. Tingapeze bwanji mphamvu pamene tafooka?

20 Ngakhale titalefuka, “ndi thandizo la Mulungu, tidzalandila mphamvu.” (Sal. 108:13) Yehova wapeleka zonse zofunika kuti mulandile mphamvu zocokela kwa iye. Conco, mukafuna thandizo kuti mucite utumiki wina wake, kupilila mayeso, kapena kukhalabe na cimwemwe, mufikileni Yehova m’pemphelo mocokela pansi pa mtima, na kufuna-funa citsogozo cake mwa kucita phunzilo la munthu mwini. Cina landilani cilimbikitso kucokela kwa Akhristu anzanu. Komanso sungani ciyembekezo canu cili cowala. Citani zimenezi kuti “mulandile mphamvu zazikulu cifukwa ca mphamvu zake zaulemelelo, kuti muthe kupilila zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso acimwemwe.”—Akol. 1:11.

NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako

a Nkhani ino idzathandiza amene amadzimvela kuti ni ofooka cifukwa ca mavuto, kapena utumiki umene aona kuti sangaukwanitse. Tidzaphunzila mmene Yehova angatilimbikitsile, komanso zimene tiyenela kucita kuti tilandile thandizo lake.

b Maina ena asinthidwa.

c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo wosakhoza kumva akuganizila malonjezo a m’Baibo, akuonelela vidiyo ya nyimbo imene ikumuthandiza kuganizila mmene umoyo wake udzakhalile m’dziko latsopano.