KHALANI MASO!
Kodi Masamba a Mcezo Akuwononga Mwana Wanu?—Mmene Baibo Ingathandizile Makolo
“Matenda a maganizo pakati pa acinyamata ni vuto lofunika kulithetsa mwamsanga, ndipo tapeza kuti kambili masamba a mcezo ndiwo amapangitsa vutoli.”—Anatelo Dokotala wamkulu wacipatala ca asilikali ku America dzina lake Dr. Vivek Murthy, mu nyuzipepala yochedwa New York Times, pa June 17, 2024.
Kodi makolo angawateteze bwanji ana awo ku zoopsa za pa masamba a mcezo? Baibo imapeleka malangizo amene angawathandize.
Zimene makolo angacite
Ganizilani mfundo za m’Baibo izi.
“Wocenjela amaganizila zotsatila za zimene akufuna kucita.”—Miyambo 14:15.
Poona kuopsa kumene kulipo, musakakamizike kulola mwana wanu kugwilitsa nchito masamba a mcezo. Musanamulole kutelo, coyamba tsimikizilani kuti ni wokhwima maganizo moti angathe kutsatila malamulo anu pa nkhani ya nthawi imene munamuikila, komanso kupitiliza kukhala na mabwenzi abwino na kupewa zosayenela.
Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?” komanso yakuti “Kuphunzitsa Mwana Wanu Wachinyamata Kukhala Wosamala Pogwiritsa Ntchito Intaneti.”
“Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:16.
Ngati mwalola mwana wanu kuseŵenzetsa masamba a mcezo, muikileni malamulo a kaseŵenzetsedwe, ndipo mufotokozeleni mmene malamulowo angamuthandizile kukhala wotetezeka. Khalani chelu kuti muone ngati mwana wanu akusintha khalidwe. Kucita izi kudzakuthandizani kuona ngati mufunika kumucepetsela nthawi yokhala pa masamba a mcezo.
Seŵenzetsani vidiyo yakuti Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti pothandiza mwana wanu kudziŵa kufunika kwa malamulo poseŵenzetsa masamba a mcezo.
Dziŵani zambili
Baibo imakamba kuti tikukhala “nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1-5) Pa nthawi imodzimodzi imapeleka malangizo amene amatithandiza kupilila. Mndandanda wa nkhani za m’Baibo zoposa 20 zothandiza makolo na ana awo upezeka mnkhani iyi yokamba za matenda a maganizo a acinyamata.