KHALANI MASO!
N’cifukwa Ciyani Cidani Caculuka?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Cidani, zaciwawa, kucitila ena nkhanza cifukwa ca mtundu wawo, komanso nkhondo ndizo nkhani zomwe zafala pa nyuzi.
“Kuposa kale lonse, nkhani za cidani zaculuka pa soshomidiya. Izi zili conco cifukwa ca nkhondo imene ikucitika pakati pa dziko la Israel na Gaza, komanso cifukwa ca anthu amene amalimbikitsa ciwawa na cidani.”—Inatelo nyuzipepala ya The New York Times, pa November 15, 2023.
“Kuyambila pa October 7 caka cino, taona kuwonjezeka kwakukulu pa nkhani ya cidani, komanso zaciwawa cifukwa cosankhana mitundu.”—Anatelo Dennis Francis, pulezidenti wa United Nations General Assembly, pa November 3, 2023.
Cidani, ciwawa, komanso nkhondo sizinayambe lelo. Baibo imakamba za anthu akale amene “[anakonzekela] kuponya mawu awo opweteka ngati mivi,” komanso amene anali kumenya nkhondo na kucita zaciwawa. (Salimo 64:3; 120:7; 140:1) Ndipo Baibo imanenanso kuti cidani cimene tikuona masiku ano cili na tanthauzo lofunika.
Cidani n’cizindikilo ca masiku athu ano
Baibo imapeleka zifukwa ziŵili zoonetsa cifukwa cake cidani cili paliponse masiku ano.
1. Inakambilatu za nthawi pamene “cikondi ca anthu ambili cidzazilala.” (Mateyu 24:12) M’malo moonetsana cikondi, anthu ambili adzakhala na makhalidwe amene amabweletsa cidani.—2 Timoteyo 3:1-5.
2. Cidani masiku ano cikuwonjezeka cifukwa ca zocita zankhanza komanso zoipa za Satana Mdyelekezi. Baibo imati “dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9, 12.
Komabe, Baibo imaonetsa kuti Mulungu adzathetsa zonse zimene zimayambitsa cidani. Koposa zonse, iye adzacotsapo mavuto onse obwela cifukwa ca cidani. Baibo imalonjeza kuti:
Mulungu “adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.