Kodi Ciukitso N’ciyani?
Yankho la m’Baibo
Mawu amene anawamasulila m’Baibo kuti ‘ciukitso,’ anacokela ku mawu acigiriki akuti a·naʹsta·sis, amene amatanthauza “kudzuka” kapena “kuimililanso.” Munthu amene waukitsidwa kwa akufa amakhalanso na moyo monga mmene analili asanamwalile.—1 Akorinto 15:12, 13.
N’zoona kuti mawu akuti “ciukitso” sapezeka m’Malemba Aciheberi, amene nthawi zambili amachedwa Cipangano Cakale. Komabe, mfundo yakuti akufa adzauka imapezeka m’malemba amenewa. Mwacitsanzo, kupitila mwa mneneli Hoseya, Mulungu analonjeza kuti: “Ine ndidzawawombola ku Manda ndiponso ku imfa.”—Hoseya 13:14; Yobu 14:13-15; Yesaya 26:19; Danieli 12:2, 13.
Kodi anthu oukitsidwa adzakhala kuti? Anthu ena akaukitsidwa, amapita kumwamba kuti akalamulile monga mafumu pamodzi na Khristu. (2 Akorinto 5:1; Chivumbulutso 5:9, 10) Baibo imati kumeneku ni “kuuka koyamba” komanso “kuuka koyambilila.” Ndipo mawu aŵili onsewa akuonetsa kuti padzakhalanso kuuka kwina. (Chivumbulutso 20:6; Afilipi 3:11) Amene adzaukitsidwa pa kuuka kwinako adzakhala ambili-mbili, ndipo adzasangalala na moyo wosatha padziko lapansi.—Salimo 37:29.
Kodi anthu adzaukitsidwa bwanji? Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsila akufa. (Yohane 11:25) Yesu adzaukitsa ‘onse amene ali m’manda acikumbutso,’ munthu aliyense monga mmene analili poyamba. (Yohane 5:28, 29) Anthu oukitsidwa kuti apite kumwamba amauka na thupi lauzimu. Koma anthu oukitsidwa kuti akhale padziko lapansi adzauka na thupi labwino, lopanda matenda komanso lopanda cilema ciliconse.—Yesaya 33:24; 35:5, 6; 1 Akorinto 15:42-44, 50.
Ndani Amene Adzaukitsidwa? Baibo imati “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Anthu olungama aphatikizapo Nowa, Sara, ndiponso Abulahamu. (Genesis 6:9; Aheberi 11:11; Yakobo 2:21) Anthu osalungama ni anthu amene sanali kutsatila mfundo za Mulungu, ndipo analibe mwayi wakuti n’kuphunzila Mawu a Mulungu na kumawatsatila.
Komabe, anthu amene amacita zinthu zoipa kwambili ndipo safuna kusintha sadzaukitsidwa. Anthu otelewo akamwalila, sayembekezela kuti angadzakhalenso na moyo.—Mateyu 23:33; Aheberi 10:26, 27.
Kodi anthu akufa adzaukitsidwa liti? Baibo inalosela kuti anthu opita kumwamba adzayamba kuukitsidwa m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu, imene inayamba mu 1914. (1 Akorinto 15:21-23) Koma anthu oukitsidwa kuti akhale na moyo padziko lapansi, adzayamba kuukitsidwa mu Ulamulilo wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu. Mu ulamulilo umenewu, dziko lapansi lidzakonzedwa kuti likhale paladaiso.—Luka 23:43; Chivumbulutso 20:6, 12, 13.
N’cifukwa ciyani n’zomveka kukhulupilila kuti akufa adzauka? M’Baibo, muli nkhani za anthu 9 amene anaukitsidwa, ndipo nkhani iliyonse imaonetsa kuti panali anthu amene anaonadi anthu oukitsidwawo. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Luka 7:11-17; 8:40-56; Yohane 11:38-44; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12; 1 Akorinto 15:3-6) Mwacitsanzo, nkhani ya Lazaro amene anaukitsidwa na Yesu ni yocititsa cidwi kwambili. Izi zili conco cifukwa patapita masiku 4 Lazaro atamwalila, Yesu anamuukitsa ndipo anthu ambili anamuona. (Yohane 11:39, 42) Ngakhale anthu amene anali kutsutsa Yesu, sanatsutse zakuti Lazaro waukitsidwa. M’malomwake, iwo anakonza ciwembu cakuti aphe Yesu na Lazaro.—Yohane 11:47, 53; 12:9-11.
Baibo imaonetsa kuti Mulungu ali na mphamvu zoukitsa akufa, komanso ali na mtima wofunitsitsa kuwaukitsa. Iye amakumbukila ciliconse cokhudza munthu aliyense amene adzamuukitsa mwa mphamvu zake zopanda malile. (Yobu 37:23; Mateyu 10:30; Luka 20:37, 38) Monga taonela, Mulungu ali na mphamvu zoukitsa akufa komanso ni wofunitsitsa kuwaukitsa. Potsimikizila zakuti anthu adzaukitsidwa m’tsogolo, Baibo imati Mulungu ‘adzalakalaka nchito ya manja ake.’—Yobu 14:15.
Maganizo olakwika pa nkhani ya ciukitso
Zimene ena amakhulupilila: Mawu akuti ciukitso atanthauza kugwilizananso kwa thupi na mzimu.
Zoona zake: Baibo imaphunzitsa kuti mzimu, kapena kuti moyo, ni munthu weniweniyo osati cinthu cinacake cimene cimakhala mwa munthu ndipo cimapitiliza kukhala na moyo munthuyo akamwalila. (Genesis 2:7; Ezekieli 18:4) Munthu akaukitsidwa sikuti thupi na mzimu wake zimagwilizanitsidwanso ayi. Koma amakhala kuti walengedwanso.
Zimene ena amakhulupilila: Anthu ena amaukitsidwa kenako n’kuwonongedwa nthawi yomweyo.
Zoona zake: Baibo imanena kuti anthu “amene anali kucita zoipa adzauka kuti aweluzidwe.” (Yohane 5:29) Iwo adzaweluzidwa potengela zimene adzacita akaukitsidwa, osati zimene anacita asanamwalile. Yesu anati: “Akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu, ndipo olabadilawo adzakhala ndi moyo.” (Yohane 5:25) Anthu amene ‘adzalabadile,’ kapena kumvela zimene adzaphunzitsidwe akadzaukitsidwa, mayina awo adzalembedwa mu “mpukutu wa moyo.”—Chivumbulutso 20:12, 13.
Zimene ena amakhulupilila: Munthu adzaukitsidwa na thupi limene anali nalo asanamwalile.
Zoona zake: Munthu akamwalila, thupi lake limawonongeka n’kusanduka dothi.—Mlaliki 3:19, 20.